CONGRATULATIONS! Woyimba “Black Nina” apambana pa Mpikisano wosankha anthu akuda khungu

Pa anthu onenepa pamakhala onenepetsa
Pa anthu ovina pamakhala ovinitsitsa
Pa anthu otchena pamakhala otchenetsa
Komanso pa anthu oyimba pamapezeka Akuda

Uyu ndi Black Nina ndipo lelo sanatchuke chifukwa cha nyimbo ayi koma khungu. Pa Mpikisano wa anthu akuda umene unaponyedwa pa tsamba la facebook la Mikozi, anthu anasankha oyimba Crispy Malawi, Tsar Leo, Phyzix, komanso Black Nina ngati anthu amene amawayimilila tikakamba za nkhani yakuda khungu.
Koma pa anthu akudawa sipalephela wowayimilia woti nawonso akamawona amalimbilapo mtima kuti “inde ine ndinada komano mzangayu amandimvetsa ngati ndine oyela”. Anthu atafunsidwa za munthu amene anadetsetsa pa anthu akuda wa, ma vote ambili anagwela “Black Nina”.

 

Black Nina ambili amamudziwa ndi nyimbo yoti “Chilawe Changachi” imene adayimba ndikulandidwa ndi Nepman. Ngakhale anazizila pakatipa, Black Nina athokoze khungu lake pomubwenzeletsa mu game.

Comments

You might also like